Apolisi kwa Jenda m’boma la Mzimba akusungira m’chitokosi a Darison Jonazi, 42, amene ndi mwini wake wa shabini ku Embangweni powaganizira kuti anadula zala zakuphazi a Molala Simwaka amene amayesa kuti ndi wakuba.
Iwo akuyembekezera kuti akayankhe mlandu wovulaza ku bwalo la milandu a Polisi akamaliza kafukufuku wawo.
Ofalitsankhani ku Polisi ya kwa Jenda, a MacFalren Mseteka, ati izi zinachitika usiku wapa 14 September chaka chino.
Patsikulo, a Simwaka anali pamodzi ndi anzawo awiri a Mavuto ndi a Roshin Simwaka amene amachokera komwa mowa m’dera la Chindoka ndipo anapitiliza kumwera panja pa shabini ya a Jonazi yomwe inali yotseka.
A Mseteka ati a Jonazi atawaona izi anayamba kumenya ndi kuvulaza anthu atatuwo ndi kudula zala zakuphazi za a Molala Simwaka zokwana zisanu kumanzere ndi chimodzi cha chikulu kuphazi lakumanja chifukwa amawona ngati amafuna awabere.
Zitachitika izi, bambowa anatengera amene anamuvulaza kwambiri ku chipatala cha Embangweni Mission kenako anamutumiza ku chipatala chachikulu cha m’bomalo komwe amalandira thandizo kufikira pa 21 September.