Malawi Broadcasting Corporation
Uncategorized

Opindula ndi Mtukula Pakhomo alandira dipo lawo pa lamya

Anthu amene akulandira ndalama za Mtukula Pakhomo m’boma la Chitipa ayamba kulandira ndalama zawo kudzera pa lamya.

Zimenezi anthuwo akuti zathandiza kuchepetsa mavuto ambiri amene amakumana nawo akapita kotenga ndalamazi kudzera ku njira ya kale.

M’mbuyomu, anthu amayenera kusonkhana ndi anzawo komanso alangizi ndi ena okhudzidwa pamalo amene awakonzera kumene amakhala pamzere ndi kumadikira kuti awayitane mayina mmodzi-mmodzi.

Iwo akuti izi zimawachotsera chinsinsi komanso zimawayika pa chiopsezo chowabera chifukwa anthu ena amadziwa ndalama zimene alandira.

M’modzi mwa opindura, a Salomy Nambeye, a zaka 47 komanso ali ndi ulumali wa miyendo, analongosola kuti ali omasuka ndi dongosolo latsopanoli.

“Kale tinkayenera kuyenda mtunda wautali kupita kumalo olipirira ndiye kwa munthu wa vuto la miyendo ngati ineyo anali mavuto aakulu kwambiri chifukwa pena amandinyamula ndi anthu kuti ndifike malo olandilira ndalama,” iwo anatero.

A Webster Songa, azaka 52 okhala m’mudzi wa kwa Mpeta m’bomali, anathira ndemanga yofanana ndi ya a Nambeye.

“Zovuta zinali zambiri, ndalama zimene timalandira zinkachepa chifukwa cha mtengo woyendera,” adatero a Songa.

Mkulu oona za chisamaliro cha anthu m’bomali, a Gladys Fatch, anayamikira dongosolo latsopanoli ponena kuti kusinthaku kupindulitsa kwambiri pulogalamuyi.

“Njira yatsopanoyi ili ndi ubwino wambiri monga apapa sipadzafunikanso kutumiza antchito kukapereka ndalama pa manja kwa opindula,” a Fatch anatero.

M’boma la Chitipa muli anthu 5, 082 amene akupindula ndi Mtukula Pakhomo.

Olemba: George Mkandawire

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

4 NATIONS TAKE TB FIGHT TO ANOTHER LEVEL

McDonald Chiwayula

Chief nabbed for flouting maize distribution exercise rules

Alinafe Mlamba

OVER 400 LEARNERS TO BENEFIT FROM STEPHANOS FOUNDATION ECD CENTRE

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.