Anthu asanu ndi awiri awatsekera ku polisi ya Ntcheu atawagwira akugulitsa mankhwala owopsa ophera tizilombo monga anankafumbwe mopanda chiloleza m’misika m’bomali.
Mmodzi wa akuluakulu ku bungwe la Pesticides Control Board, a Benson Kaphandira, ati mankhwalawa omwe ndi amapilisi komanso ena amadzi, ndi owopsa kotero kuti akuvulaza komanso kupha anthu ochuluka.
Mneneri wa apolisi ku Ntcheu, a Jacob Khembo, ati anthu omwe awamangawa, akuyankha milandu yogulitsa mankhwala owopsa popanda chilolezo komanso kugulitsa mankhwala osavomerezeka.
Iwo ati ntchitoyi ipitilira pothana ndi mchitidwewu.