Mfumu yaikulu Mwamulowe ya m’boma la Rumphi yapempha anthu omwe akukhala m’madera ena ochokera ku dera lake kuti adzikumbukira mavuto omwe ali kuderali ndikumachitapo kanthu.
Mfumuyi yayankhula izi pomwe imalandira galimoto yonyamulira matenda yomwe nzika ina yamderali yomwe ikukhala m’dziko la Australia, a Florence Khimbi, apereka.
Iwo anati a Khimbi akukumbukira mavuto omwe anthu akwawo akukumana nawo pankhani ya mayendedwe ndipo ati aka sikoyamba kuthandiza.
Masiku ambuyomu a Khimbi anapereka bwato loyendera injini lonyamuliranso matenda kwa anthu amdera la mfumuyi.
“Vuto lakuno ndi mayendedwe, odwala monga amai oyembekezera amayenda mitunda italiitali kuti apite kuchipatala kotero kuti ambiri amaberekera m’njira,” inatero Mfumu Mwamulowe.
Omwe anayimira a Khimbi pamwambowu a Macdonald Mwafulirwa anapempha mafumu kuti agwirizane pokhazikitsa njira zomwe adzigwiritsa ntchito pa galimotoyo ndi bwatolo kuti zithandize anthu amuderalo.
Olemba: Henry Haukeya