Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

Aulimali ayamika ndondomeko yopereka ndalama za mtukula pakhomo pa lamya

Anthu aulumali m’boma la Phalombe ayamika boma chifukwa choyamba kupereka ndalama za mtukula pakhomo kudzera pa lamya, zimene zathandiza kuti asamayende mtunda wa utali akafuna kulandira ndalamazi.

Polankhula ndi MBC, a Maxwell Chikopa, a m’mudzi mwa a Kazombo m’mdera la mfumu yayikulu Nkhumba m’boma la Phalombe ndipo ali ndi ulumali wa miyendo, ati zimakhala zowawa pomwe amayenda mtunda otalika makilomita 20 kuti akalandire ndalama za mtukula pankhomo.

“Pano zinthu zaphweka kwambiri chifukwa sitikuchedwa kulandira ndalama chifukwa zikalowa tikumapita kwa Agent yemwe akumatipatsa pompo pompo,” atero a Chikopa.

Nawo a George Mofolo omwe ali ndi ulumali osawona ndipo amachokera m’dera la Group Village Bwanaisa kwa mfumu yayikulu Nkhumba m’bomali, ati ndondomeko yolandira pa manja inali yowawa chifukwa amayenera kuti apeza munthu owaperekeza komanso amadikilira kwa tsiku lonse kuti alandire ndalamazi.

Mmawu ake, mkulu owona za ndondomeko ya mtukula pankhomo m’boma la Phalombo, a Fakson Chidzalo, ati ndondomeko yatsopanoyi ndiyachangu komanso akupulumutsa ndalama za nkhaninkhani zomwe amawononga pogula mafuta agalimoto komanso kulipira ogwira ntchito omwe amapita kumadera kukapeleka ndalamazi.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Triathlon Union of Malawi eyes international medals

MBC Online

Oganiziridwa za “Bakili Muluzi TV” akudikira kumva za belo

MBC Online

Mudzi wa aChewa autsekulira ku Lilongwe

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.