Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

APOLISI KU LIMBE ALONJEZA KUPEREKA CHITETEZO CHOKWANIRA

Mkulu watsopano wa Polisi ya Limbe, a Edwin Mkhambo, watsimikizira anthu ochita malonda mderali komanso madera ozungulira kuti aonetsetsa kuti kuli chitetezo chokwanira.

A Mkhambo anena izi pa msonkhano wa atolankhani komwe anatsindika kuti ntchito yoika ma camera othandizira kukhwimitsa chitetezo (CCTV camera pachingerezi), ikuthandiza kwambiri.

A Mkhambo alowa mmalo mwa a Gladwell Chipumphula, amene pano ndi wachiwiri kwa komishanala wa apolisi kuchigawo cha kummawa.

WOLEMBA: GHWABUPI ANGELA MWABUNGULU

Related posts

Apolisi agwira mbala zomwe zinaba katundu wa Radio Maria

Mayeso Chikhadzula

Musapereke za unzika kwa aliyense — Kunkuyu

Romeo Umali

Four killed in Zomba road accident

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.