Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani Sports Sports

Masewero amathandiza achinyamata kupewa khalidwe loyipa — Belekanyama

Phungu wa dera la Lilongwe Msinja South, Francis Belekanyama, watsindika zakufunika kokhazikitsa ntchito zomwe zimathandiza achinyamata kupeza zochita.

Belekanyama walankhula izi pasukulu ya pulaimale ya Matsimbe mdera lamfumu yayikulu Masula Ku Lilongwe pamwambo opereka mphoto kwa omwe apambana pamapeto pa masewero amu Belekanyama Bonanza.

Iwo anati kukhazikitsa ntchito ngati mpikisano wa mpira wamiyendo komanso wamanja zimathandiza achinyamata kupeza zochita ndikulewa makhalidwe oipa.

M’mawu ake, wapampando wachipani cha Malawi Congress (MCP) mchigawo chapakati, a Patrick Zebron Chilondola, anayamikira phunguyu pokhazikitsa zikho kudera lake.

Iwo anati phungu akakhala pampando amayenera adzigwira ntchito zotukula miyoyo ya anthu omwe anamuika pampando wake.

Pakali pano, a Belekanyama akhazikitsanso mpikisano wina wachikho cha mpira wa manja ndi miyendo cha K6 million.

#MBCDigital
#Manthu

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Chakwera lauds Speaker’s impartiality

McDonald Chiwayula

Malawi hosts Korea Cultural Festival

MBC Online

TECHNOLOGICAL CHALLENGES DELAY UNIVERSITY SELECTION RESULTS – NCHE

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.