Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Politics

Achinyamata ndi akazembe a bata, mtendere — NICE

Bungwe la National Initiative for Civic Education (NICE) lapempha achinyamata kuti akhale akazembe olimbikitsa bata ndi mtendere m’madera mwawo pamene dziko lino likuyembekezeka kuchita chisankho cha chikulu chaka cha mawa.

Bungweli lanena izi pa mwambo omema anthu a m’boma la Mangochi kuti atenge nawo mbali polembetsa m’kaundula wa voti, mugawo la kalembela wa chisankho limene likuyamba pa 28 mwezi uno m’bomali.

Mlangizi wa mkulu wa NICE m’boma la Mangochi, a Joseph Chamambala, ati kufikira achinyamata ndi uthenga wa mtendere kungathandize kwambiri chifukwa ndi anthu amene atsogoleri a ndale amawagwiritsa ntchito kuti adzichita ziwawa.

Wapampando wa gulu la mabungwe amene siaboma ku Mangochi, a Joseph Makwakwa, analonjeza kuti mabungwewa agwira ntchito limodzi ndi bungwe la NICE komanso anemema mafumu kuti alimbikitse anthu kulembetsa m’kaundula odzaponya nawo voti.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

MZUNI intensifies research

Tasungana Kazembe

MADONNA JETS IN

MBC Online

Ex-con rescued from mob amid swindling allegations

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.