Malawi Broadcasting Corporation
Crime Local News Nkhani

Apolisi agwira anthu awiri omwe akuwaganizira kuti amaba ku Area 25

Apolisi ku Lilongwe agwira anthu awiri omwe akuwaganizira kuti akukhudzidwa ndi kubedwa kwa katundu wambiri mu mzindawu komanso kuchita ziwembu.

M’neneri wa Polisi ya Kanengo, a Gresham Ngwira, ati awiriwa, a Shukulani Mussa a zaka 20 ndi ndi a Tonny Junior Juma azaka 22 akuwaganizira kuti akhala akuchita m’chitidwewu ku Area 25 B ndi madera ena ozungulira.

A Ngwira ati anthu ena akufuna kwabwino anawatsina khutu za anthuwa popeza akhala akugwiritsa ntchito ndalama mwachisawawa ndipo atafufuza anawapeza ndi katundu wambiri kuphatikizapo makanema a mtundu wa Plasma.

Awiriwa akuyembekezeka kukawonekera ku bwalo la milandu posachedwapa apolisi akamaliza kuchita kafukufuku wawo.

A Mussa amachokera m’mudzi wa Kumwembe, m’dera la mfumu yayikulu Tambala m’boma la Dedza, pomwe a Juma amachokera m’mudzi wa Mzondo m’dera la mfumu yayikulu Chitukula ku Lilongwe.

Olemba: Yamikani Makanga

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Vot Net bails out Karonga Giants FC with boots

Rudovicko Nyirenda

Artists unite to address issues affecting their welfare

Paul Mlowoka

Bushiri wagawa chimanga kwa anthu oposa 18,000

Eunice Ndhlovu
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.