Malawi Broadcasting Corporation
Agriculture Local Local News Nkhani

Aphungu akhutira ndi ntchito ya NEEF

Aphungu anyumba ya malamulo m’chigawo chapakati ayamika ntchito yogawa fetereza wangongole amene bungwe la Economic Empowerment Fund (NEEF) likupereka kwa alimi.

Mwa zina, aphunguwa amene ndi kuphatikizapo a Jephter Mwale, amenenso ndi phungu wa m’dera lapakati m’boma la Mchinji, anati akadakonda unduna oona za ulimi itsatirenso ndondomeko imene a NEEF akuchita pogawa zipangizo za ulimi zotsika mtengo mu ndondomeko ya Affordable Inputs Programme (AIP).

Pothilira ndemanga, phungu wa nyumba ya malamulo kummwera kwa boma la Mchinji, a Agness Nkusa Nkhoma, potsindika kuti ndondomeko ya AIP yakhala ili ndi zofooka koma kubwera kwa NEEF kwathandiza kusintha zinthu.

A Nkusa Nkhoma anati ngongole ya feteleza kudzera ku bungwe la NEEF ithandizira kuti dziko lino lithane ndi vuto la njala.

M’modzi mwa akuluakulu ku bungwe la NEEF, a Jacob Mderu, anati bungweli ndi lokonzeka kutumikira a Malawi munjira iliyonse m’mene boma lingakonzere kuti njala ikhale mbiri yamakedzana.

Bungwe la NEEF, pambali pogawa ndalama za ngongole zosiyanasiyana, likugawanso feteleza pafupifupi matumba 2,800 tsiku lililonse kwa alimi m’dziko muno.

Padakali pano, bungweli lagawa matumba osachepera 116000 kuyambira mwezi wa December chaka chatha.

Alimi 400,000 ndi amene akuyembekezeka kupindula ndi ngongoleyi m’dziko monse muno.

Olemba: Yamikani Makanga

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Lamulo ligwira ntchito tikakupezani mukuzembetsa fodya — Boma

MBC Online

Chakwera assures IMF, World Bank of continued sound economic policies

Mayeso Chikhadzula

Akhazikitsa chipani chatsopano

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.