Bungwe la Malawi Network of People Living with HIV and AIDS (MANET+) lapereka njinga yamoto ku ofesi ya zaumoyo ya Mzimba North yomwe ithandizire pantchito za umoyo m’bomali.
Mkulu wa bungweli, a Lawrence Khonyongwa ati njingayi ndi gawo la ntchito yaikulu yotukula zaumoyo yomwe ikulandira thandizo kuchokera kuthumba la Global Fund.
“Ili ndi gawo la chitatu la ntchito yotchedwa COVID-19 Response Mechanism yomwe cholinga chake ndikuyika dongosolo lokonzekera mavuto ena aliwonse omwe angagwe mwadzidzidzi,” anatero a Khonyongwa.
Iwo anati matenda a COVID 19 anapereka maphunziro osiyanasiyana ndikuti limodzi mwamaphuzirowa ndikukhala okonzeka.
A Khonyongwa anati njingazi azigawanso mmaboma a Likoma, Rumphi komanso Nkhotakota.
Olemba Henry Haukeya