Unduna wa zaumoyo wati kuyambira mu chaka cha 2019, anthu opitilira 3,400 amwalira m’dziko muno chifukwa chavuto la mpima.
Vuto la mpima limadza pomwe tizilombo toyambitsa matenda timasiya kufa munthu akamwa mankhwala.
Malinga ndi akatswiri azachipatala, izi zimadza kaamba kogwiritsa ntchito mankhwala molakwika, monga kuika mankhwala muzakudya za ziweto komanso pophika mowa m’makwalala, zomwe zimachititsa kuti mwanjira iliyonse anthu omwe angadye zithu zamtumduwu adye pamodzi ndi mankhwala omwe.
M’modzi mwa akuluakulu ku undunawu, Dr Gracian Harawa, walangiza anthu m’dziko muno kuti apewe mchitidwe ogwiritsa mankhwala molakwika, kunena kuti kutero kumaika miyoyo ya anthu pachiopsezo.
A Harawa anena izi ku Kamuzu Central Hospital ku Lilongwe pomwe, pamodzi ndi akuluakulu achipatalachi komanso bungwe lowona zamankhwala, amafotokozera anthu za momwe vutoli likukulira m’dziko muno.