Nduna yoona za maboma ang’ono, a Richard Chimwendo Banda, yauza mafumu kuti akhale patsogolo kuthandiza boma pantchito yothetsa katangale m’dziko muno.
A Chimwendo Banda ayankhula izi pa sukulu ya pulayimale ya Lulindo m’boma la Karonga pamwambo okweza mafumu awiri kukhala ma Sub T.A.
“Boma likayika chimanga ku ADMARC limafuna anthu adzigula mwa chilungamo osati chidzithera mavenda, komanso tikati lembani anthu ovutika tiwapatse chithandizo, mudzilemba anthu oyenera, mafumu tithandizeni,” anatero a Chimwendo Banda.
Mtemi wa Batemi Kyungu wa maboma a Karonga ndi Chitipa wati awonetsetsa kuti mafumu onse m’mabomawa akutenga gawo pothetsa katangale chifukwa amabwezeretsa chitukuko m’mbuyo.
Mafumu omwe akwezedwa m’boma la Karonga ndi Sub T.A. Mwakabanga Mwandosya ndi Sub T.A. Mwambelo.
Olemba: Musase Cheyo
Ojambula: Boston Tembo