Nduna yoona zaulimi a Sam Kawale yati anthu oposa 1.4 million ndi omwe ali mu kaundula olandira zipangizo zaulimi zotsika mtengo pa ndondomeko yaboma ya Agriculture Input Program (AIP) chaka chino.
A Kawale atsindika kuti alimi enanso ochuluka kuposa 2.4 alowa mu kaundula wa ulimi omwe apeze thandizo la ulimi logwirizana ndi mmene alili pofuna kuthandiza anthu ochuluka.
Iwo auza atolankhani ku Lilongwe kuti feteleza oposa matani 39,000 wafika kale m’dziko muno ndipo wina wafika ku madoko a Beira, Nacara ndi Dar es Salaam.
Ndunayi yati pakadali pano feteleza wafika kale kumadera ena ovuta kufika monga m’boma la Neno, ndipo maboma a Chitipa, Makanjira-Mangochi, Karonga akhala akulandira feteleza yu sabata ino ndi yamawa.
Mwazina a Kawale akuti kampani 19 ndi zomwe zagulako feteleza m’dziko muno komanso ena konkuno ku Malawi.
“Alimi okwana 6500 a mmaboma a Balaka ndi Mwanza alandira mbuzi ziwiri aliyense mundondomekoyi,” atelo a Kawale.
Chaka chino a Malawi akhoza kuona okha ngati ali nawo mundondomeko ya AIP kudzera poimba foni za manja pa *4331#.