Ogwira ntchito zofalitsankhani ku nthambi ya apolisi m’dziko muno awalimbikitsa kuti aike chidwi chachikulu pothandizira ntchito yoteteza amayi ku mchitidwe wa nkhanza mu nthawi ya chisankho.
Mkulu wa apolisi m’chigawo cha kummawa, Commissioner Barbra Mchenga Tsiga, walankhula izi ku Mangochi pamaphunziro a akuluakulu ofalitsankhani kunthambi ya polisi m’dziko muno.
Maphunzirowa, omwe akuchitika ndi thandizo lochokera ku UN Women, cholinga chake ndi kufuna kuzamitsa apolisi pa momwe angathandizire kuchepetsa nkhanza zomwe amayi komanso asungwana amakumana nazo pamene akutenga nawo mbali pachisankho.
Zina mwa nkhani zomwe zatuluka pa maphunzirowa ndizoti amayi ambiri amakumana ndi nkhanza monga kuchitidwa chipongwe mmasamba amchezo apa internet pamene akuonetsa chidwi chotenga mbali pa nkhani zachisankho, choncho ndikofunika kuti adziwe zofunika kuchita pamene akumana ndi nkhanza zotere.
Olemba: Owen Mavula