Boma lati mankhwala ophera tizilombo a chroline alibe vuto lirilonse pa umoyo ngakhalenso nkhani zokhudza ubereki.
Wachiwiri kwanduna yoona za madzi ndi ukhondo a Liana Kakhobwe Chapota anena izi pamwambo opereka mankhwala a chroline ku khonsolo ya boma la Balaka.
Ndunayi yati sizoona zomwe anthu ena akhala akunena kuti madzi omwe ayikamo mankhwala opha tizilombo monga chlorine amalepheretsa kubereka.
Mmau ake wapampando wabungwe la Evidence Action lomwe lapereka thandizoli Dr Annie Phoya ati ndicholinga cha bungweli kuthandiza Boma pa ntchito yake yopereka madzi abwino ndi aukhondo kwa a Malawi ambiri makamaka am’madera akumidzi.
Thandizoli ndila ndalama zokwana K26 million.