Malawi Broadcasting Corporation
Health Local Local News Nkhani

‘Kukwinimbira ndi vuto lalikulu m’Malawi’

Ana atatu mwa 100 alionse ndi okwinimbira m’dziko muno, kafukufuku amene achita pa sukulu ya ukachenjede ya LUANAR watsimikizira izi.

M’modzi mwa akuluakulu pa sukuluyi, a Alexander Kalimbira, amanena izi mu mzinda wa Lilongwe pa msonkhano wa adindo osiyanasiyana owunikila nkhani zakadyedwe komanso mavuto ake.

Iwo anati zimenezi zikuonetsa kuti dziko la Malawi ati silikuchita bwino pothana ndi vuto la ku kwinimbira.

Komabe a Kalimbira ati ngakhale izi zili chomwechi, dziko lino likuyesetsa kulimbana ndi vutoli kusiyana ndi momwe zinalili kale zomwe akuti ndi chizindikiro kuti kusitha kutha kukhalapo ngati adindo osiyanasiyana atatengapo gawo pothana ndi vutoli.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

COVID-19 cases now at 65 as 2 more test positive in Nkhata Bay

Alick Sambo

MHEN calls for strengthened eye health services

MBC Online

Fodya akadali ndi tsogolo lowala – Chithyola Banda

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.