Nduna yoona zachitetezo cha m’dziko, a Ken Zikhale Ng’oma, ati posachedwapa boma mogwirizana ndi dziko la China ligula zipangizo zomwe adziphunzitsira anthu amene ali ku ndende ntchito zosiyanasiyana zaluso lamanja.
Iwo adati izi zithandiza kuti akatuluka kundende adzitha kupeza zochita zowathandizira. Ndunayi yanena izi itayendera ndende ya Mzuzu.
Paulendowu zadziwikanso kuti ngakhale boma likupereka ndalama zachakudya kwa anthu amene ali ku ndende, sizikumafika msanga kaamba koti ma ofesi ena akuchedwetsa ndondomeko zina. Nkhaniyi siinasangalatse ndunayi yomwe inayimba phone pompo kuti vutoli likonzedwe.
Ndipo ndunayi yalamulanso kuti unduna wawo upereke galimoto ku ndende ya Mzuzu komwe bvuto la galimoto ndi lalikulu.
Pakadali pano, a Ng’oma apereka ndalama yokwana K1 million kuti ithandizire kumbali yachakudya pandendepo.
Olemba: Chisomo Manda