Apolisi ku Mangochi akusunga amuna anayi mchitokosi powaganizira kuti apha Isaac Mbendera wazaka 29 atamupeza akuba mbuzi mu khola.
Ofalitsa nkhani za polisi ya Mangochi a Amina Tepani Daudi atsimikiza nkhaniyi.
Amuna anayiwo ndi mwini wake wa khola a Mtenje Salanje azaka 50, a Felix Maunda azaka 45, a Shadreck Jailosi azaka 48 komanso a Christopher Mkwate azaka 48.
“Titafufuza tapeza kuti malemu Mbendera ndi anzake ena awili anathyola khola usiku ndikuba mbuzi koma eni kholalo atamva anatuluka mothandizana ndi anthu ena ndipo anagwira wakubayo ndikumumenya molapitsa” anatero Daudi.
Anthuwa akaonekera kubwalo lamilandu kukayankha mulandu wakupha.