Unduna wa zamalo wati wakwanitsa kulembera malo oposa 50,000 mukaundula wamalo a umwinimwini, pansi pa ntchito ya chitukuko cha Malawi Watershed Services Improvement Project (MWASIP) ku Chingale m’boma la Zomba.
Mmodzi wa akuluakulu mu undunawu, a Anthony Nzima, anena izi pamkumano umene anali nawo ndi olembankhani munzinda wa Blantyre.
Malinga ndi akuluakulu achitukuko cha MWASIP, ntchito yakalembera wa malo, mwazina, ikuchitika ndicholinga chofuna kubwezeretsa zachilengedwe komanso kuteteza nthaka.
Pakadali pano, a Nzima ati ntchitoyi ili mkati m’maboma a Blantyre ndi Machinga atatsiriza m’boma la Zomba.
Olemba: Simeon Shumba