Apolisi ku Mulanje akusunga m’chitokosi a Chikumbutso Sailesi a zaka 32 zakubadwa powaganizira kuti adapha mayi wina wazaka 65.
Malinga ndi ofalitsankhani wa Polisi ya Mulanje, a Leah Chagomerana, a Sailesi adawapeza atagona tulo pambali pa mtembo wa mayiwo.
A Chagomerana ati mwana wa mayiyu ndiye adawapeza anthuwa ku nyumba kwa mayi ake ndipo akuti amene akuwaganizirawa anali ataledzera, atagona cha poteropo.
A Polisi atathamangira ku nyumbayi, adawapanikiza a Sayilesi ndi mafunso ndipo iwo anati adapita ku nyumbako limodzi ndi mkazi wache komanso mzake, amene amadziwika ndi dzina lakuti ‘Yellowman’ ndipo adapha mayiwa powapotokola khosi pamene amafuna kuti abe chimanga.
Pakadali pano, a Polisi akusaka a Yellowman ndi mkazi wa a Sayilesi kuti lamulo ligwire ntchito.
Malemuwa anali a m’mudzi wa Kunkeyani kwa Mfumu yayikulu Nthiramanja m’boma la Mulanje.