Kampani yopanga mbewu ya SeedCo yalangiza alimi kuti aguliretu mbewu zovomerezeka nyengo ya dzinja isanafike.
A Dennis Mdzalimbo, omwe amaona zamalonda Ku kampaniyi anati kugula mbewu zovomerezeka kumathandiza kuti ulimi ukhale waphindu.
Iwo amayankhula izi pa msonkhano omwe anachititsa ndi anthu komanso makampani omwe amagulitsa mbewu ochokera ku chigawo cha kumpoto.
A Mdzalimbo alangizanso alimi kuti adzitsatira ulangizi wa zanyengo kuti adzibzyala mbewu zogwirizana ndi momwe mvula ikugwera.
Malingana ndi akatswiri a zanyengo, madera ena m’chigawo cha kumpoto mugwa mvula yocheperako chaka chino kamba ka mphepo yotchedwa La Nina.
Olemba: Chimwemwe Milulu