Anthu awiri avulala ku Area 4 mu mzinda wa Lilongwe pa ngozi ya galimoto yamtundu wa truck, ZA 9051, yomwe inanyamula chimanga komanso katundu wina.
Malinga ndi omwe anawona ngoziyi ikuchitika, m’modzi mwa ogwira ntchito ku ofesi za bungwe la Road Traffic and Safety Services, yemwe amayendetsa galimotoyi analephera kuimitsa galimotoyi ndipo inawomba mpanda wa kampani ya Exide Batteries yomwe ili kufupi ndi ofesi za MBC komanso Mibawa TV ndikuvulaza a Vincent Makwali omwe amachita bizinesi kuseri kwa malowa.
Malipoti akuti a bungwe la Road Traffic and Safety Services analanda galimotoyi ndi kuitengera ku office za likulu la nthambiyi ataigwira chifukwa choti inalibe zikalata zoiyenereza kuyenda pa msewu.
Padakali pano anthu omwe avulala athamangira nawo Ku chipatala.
Mneneri wa bungwe la Road Traffic Directorate, Angelina Makwecha, anati ayankhulapo za nkhaniyi kanthawi kena ponena kuti anali atatanganidwa ndi ntchito zina pomwe MBC inafuna kumva mbali ya nthambiyi pa nkhaniyi.
Olemba Yamikani Makanga