A Mtiuze Chapondera a zaka 30 am’dera la Group Village Headman Chimwendo kwa mfumu yaikulu Masumbankhunda ku Lilongwe akuti akwanitsa kuchotsa banja lawo mu umphawi wa dzaoneni kudzera mu bizinesi ya tiyi lumu yomwe anayamba m’mwezi wa October chaka chatha.
“Kapu ya tiyi yochepera ndi sikono ndimagulitsa K500 ndipo yayikulu imafika K1,100. Pa tsiku ndimapeza phindu la ndalama zoposera K12,000 zomwe zandithandiza kugula nkhumba ziwiri ndi kulima mbeu za kudimba komanso chimanga mwa zina zomwe zasintha banja langa,” watero Chapondera.
A Chapondera, amene amachita bizinesiyi pamodzi ndi amuna awo, anapeza mwayi wa mpamba oyambira bizinesiyi wa ndalama zokwana K390,000 kuchokera ku bungwe la COMSIP Cooperative Union, pansi pa ntchito yothandiza mamembala ake omwe amalandira nthandizi wa mtukula pakhomo ndi mbwezera chilengedwe, kuti atuluke mu umphawi, imene pachingerezi amayitchula kuti ‘Graduation Pilot Seed Capital’.
Pakadali pano, maanja oposera 8,000 kuchokera m’maboma 14 m’dziko muno ndiwo alandira thandizo la ndalama za mpamba wa bizinesizi.