Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

Dr Chakwera ati akufuna kubwezeretsa zomwe zinaonongeka

Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, wati chidwi chake chili pobwezeretsa zinthu zomwe anthu akhala akuononga m’buyomu kuti chuma chadziko lino chibwelere m’chimake, momwe chinalili isanafike 1994.

Mtsogoleri wa dziko linoyu wanena izi ku Area 55 ku Lilongwe pomwe amakhazikitsa ntchito yomanga malo omwe pakhale mafakitale osiyanasiyana ku Magwero.

Dr Chakwera wati mchitidwe wa andale komanso ogwira ntchito m’boma ogulitsana mafakitale aboma ndi kampani udachulukitsa umphawi m’dziko muno.

Iwo ati kupanda mafakitale kwachititsa kuti anthu asowe kogulitsa katundu wawo, dziko lidzisowa ndalama zakunja komanso mitengo ya zinthu ikwere.

Apa Dr Chakwera ati pakufunika mafakitale opanga zinthu zosiyanasiyana m’dziko muno kuti mitengo ya katundu itsike.

Iye wapempha aMalawi kuti asalimbane ndi anthu omwe anaononga koma ayende ndi omwe akufuna kukonza zomwe zinaonongeka.

Bank ya AFREXIM iyika ndalama pafupifupi K1 trillion pantchito yomanga malo a mafakitale a Magwero.

Boma lati limanganso malo onga omwewa ku Matindi ndi Chigumula ku Blantyre komanso Ku Dunduzu munzinda wa Mzuzu.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

CRWB ipereka mphoto kwa makasitomala okhulupirika

Yamikani Simutowe

Malawi Digital Network revolutionises academic research at MUBAS

MBC Online

DC issues warning to officers over work negligence

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.