Bungwe la Civil Society Elections Integrity Forum ladzudzula mmodzi mwa atsogoleri a chipani cha Democratic Progressive (DPP) a Norman Chisale kaamba ka mchitidwe olankhula mau owoopseza komanso aukali pomwe akupangitsa misonkhano.
Mkulu wa bungweli a Benedicto Kondowe ati malankhulidwe woterewa akhoza kudzagwetsa mphwayi anthu omwe akufuna kudzaponya voti pachisankho chomwe chichitike pa 16 September chaka chino.
A Kondowe anatinso powonjezera kudzetsa mantha, izi zikhoza kudzabweretsa ziwawa.
Mwazina, a Chisale, omwe ndi mkulu owona za achinyamata mchipani cha DPP, akhala akumayankhula kuti mukuona kwawo,mavoti akhoza kudzaberedwa ndipo nawonso ali ndikuthekera kobera chisankho.
Iwo akhalanso akutchula atsogoleri ena andale maina monga a Khakhakha pongotchulapo ena.
Pakadali pano, mneneri wachipani cha DPP a Shadreck Namalomba ati malankhulidwe oterewa samayimira chipani chawo kotero izi ndi zosavomerezeka konse.
A Namalomba anawonjezeranso kunena kuti atsogoleri onse andale ayenera kupewa kulankhula mawu onyoza komanso oopseza ndipo mmalo mwake ayenera kufotokoza mfundo zomwe zikhonza kukopa anthu.
Olemba: Timothy Kateta