Bungwe la Anti-Corruption Bureau (ACB) lachenjeza matimu khumi ndi awiri amene afika ndime yotsiriza yamu ligi ya Chipiku kuti asamachite katangale pamasewero awo.
Chenjezoli likudza pamene bungwe la Central Region Football Association (CRFA) Loweruka masana ku Lilongwe linayitsanitsa adindo a ACB komanso nthumwi za matimuwa pa mkumano owunikira m’mene ndime yostirizayi iyendere mopanda zachinyengo.
Mkulu oteteza m’chitidwe wa katangale ku ACB, a Susan Mtuwa Phiri, anati bungwe lawo ndi lokonzeka kulanga olakwa komanso silidzanyengelera aliyense amene adzapezele akuchita ziphuphu ndi katangale, kuphatikizirapo adindo oyendetsa ligiyi.
Mlembi wa mkulu wa CRFA, a Antonio Manda, anati salolera kuti ligiyi inyazitsidwenso ndi m’chitidwewu ngati m’mene zidakhalira chaka chatha.
A Manda anati bungwe lawo liwonetsetsa kuti ACB igwire ntchito mopanda kusokonezedwa ndi wina aliyense angakhale adindo oyendetsa ligiyi.