Apolisi kuchigawo cha ku mmawa amanga Amos Kandonje wazaka 37 pomuganizira kuti ndi mmodzi mwa mbava zomwe zinathyola nyumba ya mkulu wina wamalonda m’boma la Zomba, George Maduka, ndikuba ndalama zokwana K19 million ndi katundu wina.
Mneneri wapolisi kuchigawo chaku mmawa, Patrick Mussa, wati izi zinachitika usiku wa pa 3 April, 2024 mdera la Chinsewu mbomalo.
Malinga ndi a Mussa, mbavazo, zomwe zinali ndi zikwanje, zinaberanso anthu oyandikira nyumbayo.
A Mussa ati apolisi akwanitsa kugwira mbavayo ku Lunzu mu mzinda wa Blantyre komwe imabisala ndipo apezanso katundu wina yemwe anabedwa patsikulo, amene ndikuphatikizapo galimoto ya mtundu wa Nissan Tilda, matumba a chimanga ndi foni za mmanja.