Kampani ya Synthesis Agriculture yalangiza abusa ena kuti asiye kudalira nkhosa zawo pa umoyo wawo wa tsiku ndi tsiku ndipo m’malo mwake ayambe kugwira ntchito zaulimi kuti azidzithandiza okha.
M’modzi mwa akuluakulu ku kampaniyi a Aaron Chitimbe wati nthawi yakwana yoti abusa ayambe kudzidalira pachuma.
Iwo ati pamene abusa akuwuza anthu kuti adzapita kumwamba akuyenera kudziwanso kuti asananyamuke ulendo wakumwamba akuyenera kuti akhale ndi chakudya padziko lapansi pompano.
A Chitimbe alankhula izi pamaphunziro omwe cholinga chake ndikulimbikitsa abusa ubwino wochita ulimi pamene akukonzekera kupuma pantchito omwe akuchitikira mu mzinda wa Blantyre.
Maphunzirowa abweretsa pamodzi atumiki a Mulungu ochokera m’maboma osiyanasiyana chigawo cha kum’mwera.