Gawo lachiwiri la filimu ya “Sinister Bonds” alitulutsa pa internet kudzera ku njira ya Iplus Play.
Filimuyi yomwe ayipangira ku sukulu ya ukachenjede ya Malawi College of Accountacy motsogoleredwa ndi katswiri opanga filimu Isaac Misoya ikufotokoza za mchitidwe oyipa omwe ophunzira a msukulu za ukachenjede amatengera kwa anzawo ndipo umasokoneza maphunziro awo ndipo pofuna kupewa izi ikulimbikitsa ophunzira kuti aziganiza mozama popanga zisankho zosiyanasiyana za moyo wawo.
Ena mwa akatswiri omwe ali mu filimuyi ndi oyimba nyimbo za uzimu wodziwika Steve Wazisomo Muliya, Benson, Oscar, Chantelle komanso Smacks.
Filimu ya “Sinister Bonds” ili ndi magawo 13 omwe adzitulutsidwa pa sabata iliyonse mpaka kumapeto.