Mkulu wa timu ya Silver Strikers Patrick Chimimba wati chidwi chikhale pa zomwe Bullets yachita povomereza ndikupepesa ku timu ya Silver osati ndalama zomwe apereka.
A Chimimba auza MBC kuti makoteshoni omwe Bullets inapempha itavomera zokonzetsa bus anadutsa K10 million ndipo pakadali pano alandira K6 million.
“Mmene ndanenera nkhani ikhale zomwe Bullets yachita chifukwa ndimatimu ochepa omwe angapange izi kubwera kudzapepesa timu yomwe ayilakwira,” atero a Chimimba, poonjezera kuthokoza kwawo ku timu ya Bullets chifukwa cha kudzichepetsa.
Malinga ndi a Chimimba Bullets yawonetsa ukulu, ponena kuti ndi ochepa amabwera poyera ndikuvomera kulakwitsa kwawo.