Khonsolo ya mu mzinda wa Zomba yati ndiwokondwa kuti boma la Dr. Lazarus Chakwera tsopano laikapo chidwi pomalizitsa ntchito zachitukuko zomwe zinayamba zaima kaye kaamba kazifukwa zosiyanasiyana.
Mkulu wa khonsoloyi Archangel Bakolo anapeleka chitsanzo cha bwalo laza masewero la Zomba lomwe analiyamba mchaka cha 2017 ndi ndalama zokwana pafupi fupi K4 billio.
A Bakolo anati ndondomekoyi ikatha idzakhala itagwiritsa ndalama zokwana K15 billion.
Prezidenti wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera akuyembekezeka kuyendera ntchitozi lachisanu kuphatikizapo sukulu ya ukachenjede yosura aphunzitsi ya Domasi yomwe kupyolera ku thandizo lochokera ku dziko la Japan anawamangira nyumba yapamwamba yowerengera ndi kusungurako mabuku, zipinda zogoneramo ndi zophunzilira.
Malinga ndi mkulu wapa sukuluyi Dr. Arkanjelo Yambeni chitukuko ngati chimenechi chafika pasukulupa kaamba ka ubale wabwino wapakati pa boma la Malawi ndi dziko la Japan.