Mtsogoleri wa dziko, Dr Lazarus Chakwera, wayamikira sipika wanyumba ya malamulo, a Catherine Gotani Hara, kamba kaluntha lake potsogolera nyumbayi.
Polankhula pomwe akuwonekera mnyumbayi, Dr Chakwera wati Hara wawonetsa kusakondera komanso ukadaulo pakagwiridwe kake kantchito potsogolera nyumba ya malamulo.
Mtsogoleri wa dziko linoyu wati kamba ka utsogoleri wangwiro wa a Hara, mnyumbayi mwakhala muli bata, makamaka pa nthawi yovuta kwambiri pomwe kwakhala kusemphana maganizo kumbali ya aphungu otsutsa pa nkhani ya mtsogoleri wakumbaliyi.
Pakadali pano, President Chakwera akuyankha mafunso kuchokera kwa aphungu a mnyumbayi.