Senior Chief Inkosi Champiti ya m’boma la Ntcheu yapempha anthu m’dziko muno komanso angoni kuti asunge bata ndi mtendere pamene lero kuli mwambo woyika m’manda malemu Dr Saulos Chilima, wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino.
Iwo ati angoni ndi anthu a mtendere choncho sakufuna kumva za ziwawa zina zili zonse.
“Malemu Dr Chilima, a Bhiyeni, anali munthu wokonda mtendere choncho sitikufuna kumva zoipa zina zilizonse, angoni sayenela kugenda,” anatero Senior Chief Champiti.
Mwa zina, mfumuyi yati anthu asade nkhawa ndipo afike kudzapereka ulemu wawo otsiriza chifukwa akhazikitsa chitetezo chokwanira ngati mafumu pamodzi ndi apolisi.