Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

UTM yalimbikitsa achinyamata

Chipani cha UTM chalimbikitsa achinyamata kuti alembetse mu kaundula wa unzika kuti adzakhale ndi mwai oponya nawo voti  pachisankho chachikulu chomwe chichitike mdziko muno chaka cha mawa.

Mkulu wa achinyamata mu chipanichi a Penjani Kalua amalankhula izi ku Mangochi pa mwambo okweza mbendera ya chipanichi.

Chipani cha UTM akuti chinatsitsa mbendera yake mwezi wa June potsatira imfa ya mtsogoleri wake yemwenso anali wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino, Dr Saulos Chilima.

“Tikupempha achinyamata onse omwe akufuna kudzaponya nawo voti  kuti asachite ulesi olembetsa mkaundula wa chiphaso cha unzika ngati akufuna kudzaponya nawo voti mwezi wa September chaka cha mawa,” anatero a Kalua.

 

Olemba: Owen Mavula

Related posts

NEEF tiyithandize — Dimba

Romeo Umali

Two brothers nabbed over possessing Cannabis without permit

Romeo Umali

Malemu Lapukeni awayika lero

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.