Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Chakwera akumana ndi Papa Francis

Kazembe oyimila dziko la Malawi ku Vatican a Joseph Mpinganjira ati kukumana kwa prezidenti Dr Lazarus Chakwera ndi mtsogoleri wa mpingo wa akatolika pa dziko lonse Pope Francis, kuthandiza kulimbikitsa ubale wa maiko awiriwa komanso ndi mpingo wa akatolika pa dziko lonse.

A Mpinganjira ati dziko la Malawi lapindula kwambiri ndi ntchito zachitukuko kuphatikizapo pa zamaphunziro kuchokela ku mpingowu kuyambila kalekale ndipo ndikofunika kulimbikitsa ubalewu.

Dr Chakwera ali ku Vatican, akumananso ndi mlembi wankulu wa dziko la Vatican, asanakumana ndi akulu akulu a dziko la Italy ku Rome.

Vatican ndi dziko loima palokha lomwe mtsogoleri wake ndi Papa, lomwe liri ku Rome likulu la dziko la Italy.

Malowa anakhala likulu lampingowu kuyambila zaka zamma 4 BC atamangapo pa manda a yemwe anali ophunzira wa Yesu Khristu, Simon Petulo.

Mzinda wa Vatican uli ndi nzika zokwana pafupifupi 750 ndipo ndi okula ma hekitala 49.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

CSOs renew calls to depoliticise plane crash report

Timothy Kateta

MDF calls for improved welfare of its retirees

Trust Ofesi

‘Dziko la Mozambique ndi lofunika pa chitukoko chathu’

Secret Segula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.