Phungu wa kummwera kwa boma la Lilongwe, a Peter Dimba, wapempha mabungwe ndi aMalawi kuti agwirane manja ndi bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) pamene likupitiriza kugawa fetereza powonetsetsa kuti katunduyi wafika m’maboma ambiri mwachangu.
A Dimba ayankhula izi m’midzi ya Malingunde ndi Mpingu m’boma la Lilongwe kumene bungweli lapereka fetereza oposera matumba 500 kwa alimi.
Iwo anati ntchitoyi ili ndi kuthekera kothetsa njala m’dziko muno.
M’modzi mwa akuluakulu a bungwe la NEEF, a Kissa Kalolokesha, anati ntchitoyi ikuyenda bwino chifukwa alimi amene alandira kale fetereza wa NPK ndi UREA akupereka chilimbikitso kuti akwaniritsa masomphenya a bungweli.
A Kalolokesha analengezanso kuti NEEF yafikira alimi oposera 49,000 ndi feterezayu ndiponso alimi ochuluka ena alandira kale ngongole ya ndalama zazipangizo za ulimi zoposera K16 billion.
Mfumu yayikulu Masumbankhunda ya ku Lilongwe inalimbikitsa alimiwa kuti apewe kugulitsa feterezayu kaamba kakuti zikhoza kubwenzeretsa m’mbuyo ntchito imene boma likugwira kuti lithetse njala.
Mmbuyomu, boma linapereka K150 billion ku bungwe la NEEF ndi cholinga chakuti lipereke ngongole za zipangizo za ulimi monga fetereza m’maboma onse a m’dziko muno.
Olemba: Yamikani Makanga