Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Amuna anayi ali kundende pamulandu wakupha

Apolisi ku Mangochi akusunga amuna anayi mchitokosi powaganizira kuti apha Isaac Mbendera wazaka 29 atamupeza akuba mbuzi mu khola.

Ofalitsa nkhani za polisi ya Mangochi a Amina Tepani Daudi atsimikiza nkhaniyi.

Amuna anayiwo ndi mwini wake wa khola a Mtenje Salanje azaka 50, a Felix Maunda azaka 45, a Shadreck Jailosi azaka 48 komanso a Christopher Mkwate azaka 48.

“Titafufuza tapeza kuti malemu Mbendera ndi anzake ena awili anathyola khola usiku ndikuba mbuzi koma eni kholalo atamva anatuluka mothandizana ndi anthu ena ndipo anagwira wakubayo ndikumumenya molapitsa” anatero Daudi.

Anthuwa akaonekera kubwalo lamilandu kukayankha mulandu wakupha.

Related posts

Boma lakhazikitsa gawo lachiwiri la ntchito yolimbikitsa bata ndi mtendere

Romeo Umali

Mayiko amu Africa apilitize kugwirizana, watelo prezidenti wa dziko la Tanzania

Rabson Kondowe

MWASIP ilimbikitsa kalembera wa malo

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.