Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Dziko la Malawi tsopano liri ndi mtsogoleri wa masomphenya – Mkaka

Mlembi wa mkulu wa chipani cha MCP a Eisenhower Mkaka wati dziko la Malawi ladala chifukwa liri ndi mtsogoleri wa masomphenya.

A Mkaka anena izi ku mwambo okondwelera kuti bungwe la NEEF lakwanitsa kubwereketsa ngongole zokwana K100 billion.

Mlembiyu wati Dr Chakwera wayambitsanso sitima yofika ku Lilongwe patatha zaka 21 sitima-yi itasiya, ndipo kubweranso kwa mayendedwe apa njanji kuthandiza kuti ngongole za NEEF zipindulire anthu m’dziko muno.

Iwo ati n’chifukwa chake anthu a kwa M’baluku ku Mangochi kwa nthawi yoyamba asankha khansala wa chipani cha MCP.

Olemba: Blessings Cheleuka

Related posts

Dr Usi akhazikitsa nawo Malawi Church and Community Transformation Movement

Romeo Umali

Anthu asanu awamanga kaamba kotentha khola ndi nyumba

Rabson Kondowe

Ayamba kumanga anthu ogulitsa “ambuye tengeni”

Blessings Kanache
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.