Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Kukhala madyelero pomwe asilamu akukondwelera Eid

Pamene asilamu padziko lonse mawa pa 10 April 2024 akhale akuyembekezera kukondwelera Eid-Al-fitr, kusonyeza kumaliza kwa nyengo yakusala kudya ya Ramadan, gulu la achinyamata achisilamu la Y San Inspirations, motsogozedwa ndi Tariq Khamisa, lakonza zochitika monga zoyimbayimba zamasewero ndi madyelero ngati mbali imodzi yachikondwelerochi.

Polankhula ndi MBC, Khamisa wati akuyitana anthu osiyanasiyana osati asilamu okha ku zochitikachitikazi mumzinda wa Blantyre.

“Anthu omwe adzabwere ku mwambowu adzapindulanso pophunzitsidwa zomwe angachite pa nthawi yomwe akukumana ndi mavuto komanso momwe angagwilitsire ntchito luso lomwe ali nalo kupeza ndalama,” Watero Khamisa.

Gululi linajambula kale nyimbo ziwiri zotchedwa Moyowu ndi Shukura, zomwe cholinga chake ndikupereka chilimbikitso kwa anthu omwe akukumana ndi mavuto osiyanasiyana, kuphatikizapo omwe ali ndi malingaliro ofuna kuzipha.

 

Related posts

Government conducts outreach initiative at KCH

Romeo Umali

TNM donates K3 million towards business journalists’ AGM

Romeo Umali

Residents concerned over waste accumulation at Karonga Main Market

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.