Mwambo omwe bungwe loyendetsa masewero ampira wa miyendo mu ligi yaikulu ya dziko lino wayamba munzinda wa Lilongwe.
Malinga ndi mtsogoleri wa SULOM, a Gilbert Mitawa, bungweli likuyembekeza kutolera ndalama zosachepera K150 million kuti zithandizire kuyendetsera ligi.
“Ndalamazi zimathandiza kulipira oyimbira mpira, mwazina,” atero a Mitawa.
Pamwambowu pabwera mkulu oyimira boma pamilandu a Thabo Chakaka Nyirenda, mtsogoleri wa Football Association of Malawi Fleetwood Haiya, akatakwe akale pachikopa komanso mkulu pankhani zamalonda, a Thomson Mpinganjira.