Bungwe loona zisankho m’dziko muno la MEC lati opikisana pa chisankho amaoneka papepala loponyera voti potengera zilembo zoyambilira za maina awo osati chipani chomwe akuyimira pa chisankho.
Pa chifukwa ichi, bungweli latsutsa zomwe ena akunena kuti lasankha munthu wina komanso likufuna kuti munthu yemwe akuyimira chipani china adzapambane pa chisankho chapadera cha khansala m’dera la Mwansa m’boma la Mangochi.
Bungweli lichititsa chisankho chapadera ku Mwansa pa 23 mwezi uno.
Chikalata chomwe MEC yatulutsa ndipo wasayinira ndi mkulu ofalitsa nkhani za bungweli a Sangwani Mwafulirwa chapempha omwe akupikisana pa chisankhochi, zipani zandale ndi ozitsatira kuti atsatire malamulo a chisankho omwe anasayinira.
A Mwafulirwa ati “Atsogoleri a zipani akupemphedwa kukopa anthu powauza mfundo zomveka osati kumawauza zinthu zabodza”.
Bungweli lakumbutsa anthu kuti silitumikira chipani chilichonse koma ntchito yake ndi kuchititsa chisankho mokomera anthu onse.
Olemba: Kondwani Chinele