Ntchito yoponya voti pachisankho chapadera chosankha khansala wa dera la Mwasa ili mkati m’boma la Mangochi.
Pamene imakwana 5:30 m’mawa, anthu ochuluka anayamba kufika pamalo oponya voti pa sukulu ya pulaimare ya St St Augustine 3.
Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) likuchititsa chisankho chapaderachi potsatira imfa ya yemwe anali khansala waderali malemu Edna Yusuf Jose m’chaka cha 2022.
Pakadali pano, Komishonala wa bungwe la MEC, a Richard Chapweteka, ati bungweli ndi lokhutira ndi momwe ntchito yoponya voti yayambira.
Olemba: Owen Mavula