Katswiri pa utsogoleri ndi ufulu wa anthu, a Undule Mwakasungula, ati kusankhidwa kwa Justice Annabel Mtalimanja ngati wapampando wa bungwe la MEC ndi chilimbikitso kwa amai ndi atsikana m’dziko muno.
A Mwakasungula ati izi zawonetsa chidwi cha mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera chokweza amayi m’maudindo osiyanasiyana.
Justice Annabel Mtalimanja awasankha kulowa mmalo mwa Justice Dr. Chifundo Kachale omwe nthawi yawo yogwira ntchito pa mpandowu yatha.
Olemba: Blessings Cheleuka