Bungwe la Malawi Bureau of Standards (MBS) latsegulanso sitolo ya Ekhaya ya ku Kanengo mu mzinda wa Lilongwe.
Lolemba, bungweli linatseka sitoloyi ndi zina zinayi kaamba kosatsatira ndondomeko za ukhondo zimene bungweli linakhazikitsa.
Kutsatira izi, ofalitsa nkhani ku MBS, a Wazamazama Katatu, anapempha eni sitolo m’dziko muno kuti malo awo adzikhala aukhondo.
A Katatu ati tsopano eni sitolo zimene anazitseka ayamba kukonza sitolo zawo malinga ndi m’ndandanda wa mavuto awo ndipo akufikira bungweli kuti liwayendere kuwaunika ngati akwaniritsa ndondomekozi ndi kuwatsegulira.
Iwo anati eni sitolozi akupereka chindapusa ngati chenjezo komanso phunziro kuti asadzachitenso izi.
Pakadalipano, m’modzi mwa akuluakulu a sitolo za Ekhaya, a Fanwell Khuluza, ati izi zawaphunzitsa ndipo aonetsetsa kuti sitolo za Ekhaya zikutsata ndondomeko zonse za MBS.