Mphunzitsi watsopano wa timu ya Mighty Wanderers, Nsanzurwimo Ramadhan, wachenjeza matimu m’dziko muno kuti akonzekere kuchita wefuwefu chifukwa athamanga ngati akufuna afanane ndi ukadaulo wake.
Ramadhan wanena izi pabwalo la ndege la Chileka mumzinda wa Blantyre pofika m’dziko muno kuchokera m’dziko la Tanzania.
Ramadhan anakhalako mphunzitsi wa timu ya dziko lino ya The Flames komanso FCB Nyasa Big Bullets.
Malinga ndi bungwe la FAM,ligi ya masewero a mpira wa miyendo m’dziko muno iyamba mmwezi wa April.
#MBCOnlineServices