Mkulu ozenga milandu yaboma, a Masauko Chamkakala
Komiti yakunyumba yamalamulo yoona zamalamulo yati yagwirizana ndi zifukwa zomwe mkulu ozenga milandu yaboma, a Masauko Chamkakala, anaathetsera mlandu wa wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino, Dr Saulos Chilima.
Iwo ati mlanduwu umakhudza chitetezo chadziko ndipo sungabwelere kubwalo lamilandu.
Malinga ndi wapampando wakomitiyi, a Peter Dimba, mlandu omwe ubwelere kubwalo lamilandu pakadali pano omwe mkulu ozenga milandu yaboma m’dziko munoyu adaauthetsa ndiokhudza kampani ya Paramount Holdings.
A Dimba ati umboni omwe a Chamkakala anafotokozera komitiyi kuti athetse mlandu okhudza kampaniyi siogwirika.
Akuluakulu a kampani ya Paramount Holdings amkawaimba mlandu opereka zikalata zabodza kuti apeze mwayi operekera katundu ku nthambi komanso maunduna ena aboma, pomwe wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino amkamuimba mlandu okhudzana ndi katangale.