Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani

Illovo ithandiza okhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi ku Nkhotakota

Anthu amene anakhudzidwa ndi ngozi ya kusefukira kwa madzi chaka chino ku Dwangwa m’boma la Nkhotakota alandira katundu osiyanasiyana wa ndalama zokwana K100 million kuchokera ku kampani ya Illovo sugar.

Loya wa kampani ya Illovo, yemwenso amayang’anira zofalitsankhani, a Maureen Kachingwe, anati anapeza thandizoli kuchokera ku South Africa ndi maiko ena a ku Ulaya.

M’modzi mwa akuluakulu ku kampaniyi, a Jeromy Ngolombe, apemphanso anthu okhudzidwa kuti alimbikitse ntchito zobzyala mitengo, zomwe ati zili ndi kuthekera kobwezeretsa chilengedwe m’dziko muno.

Wina mwa katundu yemwe apereka ndi zofunda, mapoto komanso zakudya.

Anthu asanu ndi omwe anamwalira pa ngoziyi ndipo anthu oposa 14,000 ndi amene anakhudzidwa ndi madzi osefukirawa m’mwezi wa February chaka chino.

Olemba: Thokozani Jumpha

Related posts

FAM dates coaches ahead of new season

Romeo Umali

MET warns about Mwera winds on Lake Malawi

Romeo Umali

Sho Madjozi to perform at 2024 Lake of Stars Arts festival

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.