Prezidenti wa dziko lino, Dr. Lazarus Chakwera ndi Mayi wa dziko lino, Madam Monica Chakwera, ati ndi okhudzika kwambiri ndi imfa ya mtsogoleri wa mpingo wa Katolika pa dziko lonse, Papa Francis.
Chikalata chomwe atulutsa, Dr. Chakwera wati anali ndi mwayi okumana ndi mtsogoleriyu miyezi isanu ndi inayi yapitayi ndipo wati Papa Francis wasiya mbiri yabwino yolimbikitsa chikhulupiliro,chikondi, kudzipereka komanso kulimbikitsa mtendere,chilungamo ndi umodzi.
Prezidenti Chakwera wati Papa Francis adzakumbukiridwa pa chidwi chake cholimbikitsa utsogoleri wabwino, omwe iye anali chitsanzo posintha mayendetsedwe a mpingo wa Katolika mu njira zosiyanasiyana.
Apa Dr.Chakwera ndi Madam Monica Chakwera apepesa akubanja la Papa Francis, akhristu a mpingo wa Katolika kuno ku Malawi ndi dziko lonse pa Imfayi.