Apolisi ku Lilongwe amanga a Symon Josephy, 35, powaganizira kuti anagwililira mwana wa zaka zisanu ndi zinayi (9) yemwenso ndi mchemwali wa mkazi wa bamboyo.
Wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za polisi ya Lilongwe, a Khumbo Sanyiwa, ati bamboyo anapita komwa mowa kumene anabwerako usiku ndipo atafika anapeza mkazi wake wagona. Kenako anapita kuchipinda komwe amagona mwanayo ndi kumugwililira.
A Sanyiwa anati mkazi wa bamboyo atapita ku chipinda cha mwanayo kuti akamuone, anadabwa kuti mwanayo wagwiliridwa. Atamufunsa, bamboyo anavomera kuti wachita izi ndi iyeyo.
A Josephy amachokera m’mudzi wa Sitenala, mfumu yaikulu Mpemba ku Dedza ndipo akaonekera kubwalo lamilandu posachedwapa pa mlandu ogwililira.